Malachi 3:1 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chauta Wamphamvuzonse akunena kuti, “Ndidzatuma wamthenga wanga kuti akandikonzere njira. Kenaka mwadzidzidzi Chauta amene mukumfunafuna adzafika ku Nyumba yake. Wamthenga wa chipangano, amene mukumuyembekeza, suuyu akubwera.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Taonani, ndituma mthenga wanga, kuti akonzeretu njira pamaso panga; ndipo Ambuye amene mumfuna adzadza ku Kachisi wake modzidzimutsa; ndiye mthenga wa chipangano amene mukondwera naye; taonani akudza, ati Yehova wa makamu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yehova Wamphamvuzonse akuti, “Ine ndidzatuma mthenga wanga amene adzakonza njira pamaso panga. Kenaka mwadzidzidzi Ambuye amene mukumufunafuna adzafika ku Nyumba yake. Mthenga wapangano amene mukumuyembekezera adzabwera.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Taonani, ndituma mthenga wanga, kuti akonzeretu njira pamaso panga; ndipo Ambuye amene mumfuna adzadza ku Kacisi wace modzidzimutsa; ndiye mthenga wa cipangano amene mukondwera naye; taonani akudza, ati Yehova wa makamu.