Malachi 3:14 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mwanena kuti, ‘Kutumikira Mulungu nkwachabe. Kodi pali phindu lanji kumatsata malamulo a Chauta Wamphamvuzonse, kapena kumaonetsa chisoni pamaso pake?
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Mwanena, Kutumikira Mulungu nkwa chabe; ndipo tapindulanji ndi kusunga udikiro wake, ndi kuyenda ovala zamaliro pamaso pa Yehova wa makamu?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Mwanena kuti, ‘Kutumikira Mulungu nʼkosapindulitsa. Kodi timapindulanji pochita zofuna zake, ndi kumayenda ngati anamfedwa pamaso pa Yehova Wamphamvuzonse?
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Mwanena, Kutumikira Mulungu nkwa cabe; ndipo tapindulanji ndi kusunga udikiro wace, ndi kuyenda obvala zamaliro pamaso pa Yehova wa makamu?