Malachi 3:16 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono oopa Chauta adayamba kukambirana, Chauta namamvetsera. Buku lachikumbutso lidalembedwa pamaso pake, lonena za amene ankaopa Chauta ndi kulemekeza dzina lake.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamenepo iwo akuopa Yehova analankhulana wina ndi mnzake; ndipo Yehova anawatchera khutu namva, ndi buku la chikumbutso linalembedwa pamaso pake, la kwa iwo akuopa Yehova, nakumbukira dzina lake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo woopa Yehova anayamba kukambirana, ndipo Yehova anamvetsera. Buku la chikumbutso linalembedwa pamaso pake, lonena za amene amaopa Yehova ndi kulemekeza dzina lake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamenepo iwo akuopa Yehova analankhulana wina ndi mnzace; ndipo Yehova anawachera khutu namva, ndi buku la cikumbutso linalembedwa pamaso pace, la kwa iwo akuopa Yehova, nakumbukila dzina lace.