Malachi 3:17 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chauta Wamphamvuzonse akunena kuti, “Anthu amenewo adzakhala anga, adzakhala angaanga okondedwa pa tsiku limene ndidzalikonza. Ndidzaŵachitira chifundo monga m'mene munthu amachitira ndi mwana wake womtumikira.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo adzakhala angaanga, ati Yehova wa makamu, tsiku ndidzaikalo, ndipo ndidzawaleka monga munthu aleka mwana wake womtumikira.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yehova Wamphamvuzonse akuti, “Anthu amenewo adzakhala anga, tsiku limene Ine ndidzachita izi, adzakhala angaanga. Ndidzawaleka osawalanga monga mmene munthu amachitira chifundo mwana wake amene amamutumikira.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo adzakhala anga anga, ati Yehova wa makamu, tsiku ndidzaikalo, ndipo ndidzawaleka monga munthu aleka mwana wace womtumikira.