Malachi 3:2 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kodi ndani adzatha kupirira pa tsiku la kubwera kwake? Kodi ndani adzatha kulimbikira iye akadzafika? “Pakuti adzakhala ngati moto wa mmisiri wapang'anjo, ndiponso ngati sopo wa munthu wochapa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma ndani adzapirira tsiku la kudza kwake? Ndipo adzaima ndani pooneka Iye? Pakuti adzanga moto wa woyenga, ndi sopo wa otsuka;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma ndani adzatha kupirira pa tsiku la kubwera kwake? Ndani adzatha kuyima pamene Iye wafika? Pakuti adzakhala ngati moto wa mmisiri wa pa ngʼanjo, kapenanso ngati sopo wa munthu wochapa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma ndani adzapirira tsiku la kudza kwace? ndipo adzaima ndani pooneka Iye? pakuti adzanga moto wa woyenga, ndi sopo wa otsuka;