Malachi 3:7 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kuyambira masiku a makolo anu mwakhala mukuphwanya malamulo anga, simudaŵatsate konse. Ngati mubwerera kwa Ine, Inenso ndidzabwerera kwa inu. Ndikutero Ine Chauta Wamphamvuzonse. Komabe inu mumati, ‘Kodi tingathe kubwerera bwanji?’
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Kuyambira masiku a makolo anu mwapatuka kuleka malemba anga osawasunga. Bwererani kudza kwa Ine, ndipo Ine ndidzabwerera kwa inu, ati Yehova wa makamu. Koma inu mukuti, Tibwerere motani?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kuyambira nthawi ya makolo anu mwakhala mukuphwanya malamulo anga ndipo simunawatsatire. Bwererani kwa Ine, ndipo Ine ndidzabwerera kwa inu,” akutero Yehova Wamphamvuzonse. “Koma inu mukufunsa kuti, ‘Tibwerere motani kwa Yehova?’
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Kuyambira masiku a makolo anu mwapambuka kuleka malemba anga osawasunga. Bwererani kudza kwa Ine, ndipo Ine ndidzabwerera kwa inu, ati Yehova wa makamu. Koma inu mukuti, Tibwerere motani?