Malachi 3:8 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ine ndikuti, Kodi munthu angathe kubera Mulungu? Komabe inu mumandibera. Inu mumati, ‘Kodi timakuberani bwanji?’ Ine ndikuti, Mumandibera pa zachikhumi zanu ndi zopereka zina.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Kodi munthu adzalanda za Mulungu? Ndipo inu mundilanda Ine. Koma mukuti, Takulandani zotani? Limodzilimodzi la magawo khumi, ndi zopereka.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Kodi munthu angathe kuba za Mulungu? Komatu inu mumandibera. “Koma inu mukufunsa kuti, ‘Kodi timakuberani motani?’ “Pa zakhumi ndi pa zopereka.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Kodi munthu adzalanda za Mulungu? ndipo inu mundilanda Ine. Koma mukuti, Takulandani zotani? Limodzi limodzi la magawo khumi, ndi zopereka.