Malachi 4:1 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chauta Wamphamvuzonse akunena kuti, “Tsiku likubwera pamene anthu onse odzikuza ndi ochita zoipa adzapsa ngati chiputu m'ng'anjo. Tsiku limenelo adzapserereratu osatsalako muzu kapena nthambi. Ndikutero Ine Chauta Wamphamvuzonse.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti taonani, likudza tsiku, lotentha ngati ng'anjo; ndipo onse akudzikuza ndi onse akuchita choipa. Adzakhala ngati chiputu; ndi tsiku lilinkudza lidzawayatsa, ati Yehova wa makamu, osawasiyira muzu kapena nthambi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yehova Wamphamvuzonse akuti, “Ndithu tsiku likubwera; lidzayaka ngati ngʼanjo. Anthu onse odzikuza, ndi aliyense ochita zoyipa adzapsa ngati chiputu, ndipo pa tsiku limene likubweralo adzapserera ndi moto. Sipadzatsalira muzu kapena nthambi.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti taonani, likudza tsiku, lotentha ngati ng'anjo; ndipo onse akudzikuza ndi onse akucita coipa, adzakhala ngati ciputu; ndi tsiku lirinkudza lidzawayatsa, ati Yehova wa makamu, osawasiyira muzu kapena nthambi.