Malachi 4:2 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma inu amene mumaopa dzina langa, dzuŵa lachilungamo lidzakutulukirani lili ndi kuŵala kokuchiritsani. Mudzalumphalumpha mokondwa ngati ana a ng'ombe ochokera m'khola.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma inu akuopa dzina langa, dzuwa la chilungamo lidzakutulukirani, muli kuchiritsa m'mapiko mwake; ndipo mudzatuluka ndi kutumphatumpha ngati anaang'ombe onenepa otuluka m'khola.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma inu amene mumaopa dzina langa, dzuwa lachilungamo lidzakutulukirani lili ndi kuwala kokuchiritsani. Ndipo inu mudzatuluka ndi kulumphalumpha ngati ana angʼombe amene atulutsidwa mʼkhola.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma inu akuopa dzina langa, dzuwa la cilungamo lidzakuturukirani, muli kuciritsa m'mapiko mwace; ndipo mudzaturuka ndi kutumphatumpha ngati ana a ng'ombe onenepa,