Mark 1:16 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pamene Yesu ankayenda m'mbali mwa nyanja ya Galileya, adaona anthu aŵiri, Simoni ndi mbale wake Andrea, akuponya khoka m'nyanjamo, popeza kuti anali asodzi.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo pakuyenda m'mbali mwa nyanja ya Galileya, anaona Simoni ndi Andrea, mbale wake wa Simoni, alinkuponya khoka m'nyanja; pakuti anali asodzi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pamene Yesu ankayenda mʼmbali mwa nyanja ya Galileya, anaona Simoni ndi mʼbale wake Andreya akuponya khoka mʼnyanja, popeza anali asodzi.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo pakuyenda m'mbali mwa nyanja ya Galileya, anaona Simoni ndi Andreya, mbale wace wa Simoni, alinkuponya psasa m'nyanja; pakuti anali asodzi.