Mark 1:34 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Yesu adachiritsa ambiri amene ankavutika ndi matenda osiyanasiyana, ndipo adatulutsa mizimu yoipa yambiri. Koma mizimuyo ankailetsa kuti isalankhule, chifukwa idaamzindikira.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anachiritsa anthu ambiri akudwala nthenda za mitundumitundu, natulutsa ziwanda zambiri; ndipo sanalole ziwandazo zilankhule, chifukwa zinamdziwa Iye.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yesu anachiritsa ambiri amene anali ndi matenda osiyanasiyana, komanso anatulutsa ziwanda zambiri, ndipo sanalole kuti ziwandazo ziyankhule chifukwa zinkamudziwa Iye.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anaciritsa anthu ambiri akudwala nthenda za mitundu mitundu, naturutsa ziwanda zambiri; ndipo sanalola ziwandazo zilankhule, cifukwa zinamdziwa Iye.