Mark 1:38 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma Iye adaŵauza kuti, “Tiyeni tinke ku midzi ina kufupi konkuno, ndikalalike mau kumenekonso, pakuti ndizo ndidadzera.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo ananena nao, Tiyeni kwina, kumidzi ili pafupi apa, kuti ndilalikire komwekonso; pakuti ndadzera ntchito imene.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yesu anayakha kuti, “Tiyeni tipite kwina ku midzi ya pafupi kuti ndikalalikirenso kumeneko. Ichi ndi chifukwa chimene ndinabwerera.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ananena nao, Tiyeni kwina, ku midzi iri pafupi apa, kuti ndilalikire komwekonso; pakuti ndadzera nchito imene.