Mark 1:44 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Adati, “Chenjera, usakambire wina aliyense zimenezi. Ingopita, ukadziwonetse kwa wansembe, ndipo ukapereke nsembe adalamula Mose ija. Imeneyo ikhale yotsimikizira anthu onse kuti wachiradi.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
nanena naye, Ona, usati unene kanthu kwa munthu aliyense: koma muka, ukadzionetse kwa wansembe, nupereke pa makonzedwe ako zimene adalamulira Mose, zikhale mboni kwa iwo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Wonetsetsa kuti usawuze aliyense za zimenezi. Koma pita, kadzionetse wekha kwa wansembe ndi kukapereka nsembe zimene Mose analamulira zotsimikizira kuyeretsedwa kwanu, ngati umboni kwa iwo.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
nanena naye, Ona, usati unene kanthu kwa munthu ali yense: koma muka, ukadzionetse kwa wansembe, nupereke pa makonzedwe ako 1 zimene adalamulira Mose, zikhale mboni kwa iwo.