Mark 1:5 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Anthu ochokera ku dera lonse la Yudeya ndi a ku Yerusalemu ankadza kwa iye. Tsono ankati iwo akaulula machimo ao, iye nkumaŵabatiza mu Mtsinje wa Yordani.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anatuluka a ku dziko lonse la Yudeya, ndi a ku Yerusalemu onse; nadza kwa iye nabatizidwa ndi iye mumtsinje Yordani, powulula machimo ao.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Madera onse a ku Yudeya ndi anthu onse a ku Yerusalemu anatuluka napita kwa iye. Akavomereza machimo awo, amawabatiza mu mtsinje wa Yorodani.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anaturuka a ku dziko lonse la Yudeya, ndi a ku Yerusalemu onse; nadza kwa iye nabatizidwa ndi iye mumtsinje Yordano, poulula macimo ao.