Mark 10:1 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Yesu adachoka ku Kapernao, napita ku dera la ku Yudeya ndi ku dera la kutsidya kwa mtsinje wa Yordani. Anthu ambirimbiri adadzasonkhananso kwa Iye, ndipo monga ankazoloŵera, adayambanso kuŵaphunzitsa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo ananyamuka Iye kumeneko, nadza ku maiko a ku Yudeya ndi ku tsidya lija la Yordani; ndipo anasonkhananso kwa Iye makamu a anthu; ndipo monga anazolowera, anawaphunzitsanso.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo Yesu anachoka pamalowo ndi kupita kudera la Yudeya ndi kutsidya la mtsinje wa Yorodani. Magulu a anthu anabweranso kwa Iye, ndipo monga mwachizolowezi chake anawaphunzitsa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ananyamuka Iye kumeneko, nadza ku maiko a ku Yudeya ndi ku tsidya lija la Yordano; ndipo anasonkhananso kwa Iye makamu a anthu; ndipo monga anazolowera, anawaphunzitsanso.