Mark 10:17 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pamene Yesu ankanyamuka kuti azipita, munthu wina adamthamangira. Adadzamugwadira namufunsa kuti, “Aphunzitsi abwino, kodi ndizichita chiyani kuti ndikalandire moyo wosatha?”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo pamene Iye anatuluka kutsata njira, anamthamangira munthu, namgwadira Iye, namfunsa, Mphunzitsi wabwino, ndidzachita chiyani kuti ndilandire moyo wosatha?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yesu atanyamuka, munthu wina anamuthamangira nagwa mogwada pamaso pake. Iye anafunsa kuti, “Aphunzitsi abwino, ndichite chiyani kuti ndilandire moyo wosatha?”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo pamene Iye anaturuka kutsata njira, anamthamangira munthu, namgwadira Iye, namfunsa, Mphunzitsi wabwino, ndidzacita ciani kuti ndilandire moyo wosatha?