Mark 10:33 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Adati, “Tilitu pa ulendo wa ku Yerusalemu. Kumeneko Mwana wa Munthu akukaperekedwa kwa akulu a ansembe ndi aphunzitsi a Malamulo. Iwo akamuweruza ndi kugamula kuti aphedwe. Ndipo akampereka kwa anthu akunja.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
nati, Taonani, tikwera ku Yerusalemu; ndipo Mwana wa Munthu adzaperekedwa kwa ansembe aakulu ndi alembi; ndipo iwo adzamweruza kuti ayenera imfa, nadzampereka Iye kwa anthu a mitundu;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iye anati, “Ife tikupita ku Yerusalemu ndipo Mwana wa Munthu adzaperekedwa kwa akulu a ansembe ndi aphunzitsi amalamulo. Adzamuweruza kuti aphedwe ndipo adzamupereka kwa anthu a mitundu ina,
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
nati, Taonani, tikwera ku Yerusalemu; ndipo Mwana wa munthu adzaperekedwa kwa ansembe akuru ndi alembi; ndipo iwo adzamweruza kuti ayenera imfa, nadzampereka Iye kwa anthu a mitundu;