Mark 10:40 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma Ineyo si udindo wanga kusankha munthu kuti akhale ku dzanja langa lamanja, kapena ku dzanja langa lamanzere. Mulungu ndiye adzapereke malo ameneŵa kwa omwe Iye mwini adaŵakonzera.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
koma kukhala kudzanja langa lamanja, kapena lamanzere sikuli kwanga kupatsa; koma kuli kwa iwo amene adawakonzeratu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
koma kukhala kumanja kapena kumanzere si Ine wopereka. Malo awa ndi a amene anasankhidwiratu.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
koma kukhala ku dzanja langa lamanja, kapena kulamanzere sikuli kwanga kupatsa; koma kuli kwa iwo amene adawakonzeratu,