Mark 10:46 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Yesu ndi ophunzira ake pamodzi ndi gulu lalikulu la anthu adafika ku mzinda wa Yeriko. Tsono pamene ankatuluka mumzindamo, adapeza wakhungu wina wopemphapempha atakhala pansi pamphepete pa mseu. Munthuyo dzina lake anali Baratimeo, mwana wa Timeo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo iwo anafika ku Yeriko; ndipo m'mene Iye analikutuluka m'Yeriko, ndi ophunzira ake, ndi khamu lalikulu la anthu, mwana wa Timeo, Baratimeo, wopempha wakhungu, analikukhala pansi m'mbali mwa njira.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo anafika ku Yeriko. Pamene Yesu ndi ophunzira ake, pamodzi ndi gulu lalikulu la anthu, ankatuluka mu mzinda, munthu wosaona, Bartumeyu (mwana wa Tumeyu), amakhala mʼmbali mwa msewu ali kupempha.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo iwo anafika ku Yeriko; ndipo m'mene Iye analikuturuka m'Yeriko, ndi ophunzira ace, ndi khamu lalikuru la anthu, mwana wa Timeyu, Bartimeyu, wopempha wakhungu, analikukhala pansi m'mbali mwa njira.