Mark 11:15 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Iwo adafika ku Yerusalemu. Tsono Yesu adaloŵa m'Nyumba ya Mulungu, nayamba kutulutsa anthu amene ankachita malonda m'menemo. Adagubudula matebulo a osinthitsa ndalama, ndi mipando ya ogulitsa nkhunda.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anafika iwo ku Yerusalemu; ndipo Iye analowa m'Kachisi, nayamba kutulutsa akugulitsa ndi akugula malonda m'Kachisimo, nagubuduza magome a osinthana ndalama, ndi mipando ya ogulitsa nkhunda;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Atafika ku Yerusalemu, Yesu analowa mʼbwalo lakunja la Nyumba ya Mulungu ndipo anayamba kupirikitsa anthu amene amagula ndi kugulitsa mʼmenemo. Anagubuduza matebulo a osintha ndalama ndi mipando ya ogulitsa nkhunda,
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anafika iwo ku Yerusalemu; ndipo Iye analowa m'Kacisi, nayamba kuturutsa akugulitsa ndi akugula malonda m'Kacisimo, nagubuduza magome a osinthana ndalama, ndi mipando yaogulitsa nkhunda;