Mark 11:18 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Akulu a ansembe ndi aphunzitsi a Malamulo atamva zimenezi, adayamba kufunafuna njira yoti amuphere. Pakutitu ankachita naye mantha poona kuti anthu onse ankadabwa nazo zimene Iye ankaphunzitsa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo ansembe aakulu ndi alembi anamva, nafunafuna momuonongera Iye; pakuti anamuopa, chifukwa khamu lonse la anthu linazizwa ndi chiphunzitso chake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Akulu a ansembe ndi aphunzitsi amalamulo anamva izi ndipo anayamba kufuna njira yoti amuphere Iye, pakuti amamuopa, chifukwa gulu lonse la anthu linazizwa ndi chiphunzitso chake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ansembe akuru ndi alembi anamva, nafunafuna momuonongera Iye; pakuti anamuopa, cifukwa khamu lonse la anthu linazizwa ndi ciphunzitso cace.