Mark 11:2 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
naŵauza kuti, “Pitani m'mudzi mukuwonawo. Mukangoloŵamo, mukapeza mwanawabulu ali chimangire, amene munthu sanakwerepo chikhalire. Mukammasule nkubwera naye.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
nanena nao, Mukani, lowani m'mudzi wapandunji ndi inu; ndipo pomwepo pakulowamo mudzapeza mwana wa bulu womangidwa, amene palibe munthu anakhalapo kale lonse; mmasuleni, ndipo mubwere naye.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
nati kwa iwo, “Pitani ku mudzi uli patsogolo panu, ndipo mukamakalowa, mukapeza mwana wabulu atamangiriridwa pamenepo, amene wina aliyense sanakwerepo. Kamumasuleni ndi kubwera naye kuno.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
nanena nao, Mukani, lowani m'mudzi wapandunji ndi inu; ndipo pomwepo pakulowamo mudzapeza mwana wa buru womangidwa, amene palibe munthu anakhalapo kale lonse; mmasuleni, ndipo mubwere naye.