Mark 11:23 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndithu ndikunenetsa kuti aliyense wolamula phiri ili kuti, ‘Choka apa, kadziponye m'nyanja,’ atanena ndi mtima wosakayika, nakhulupirira ndithu kuti zimene akunenazo zichitikadi, ndithu zidzachitikadi monga momwe waneneramo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndithu ndinena ndi inu, kuti, Munthu aliyense akanena ndi phiri ili, Tanyamulidwa, nuponyedwe m'nyanja; wosakayika mumtima mwake, koma adzakhulupirira kuti chimene achinena chichitidwa, adzakhala nacho.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Zoonadi, Ine ndikuwuzani kuti ngati wina aliyense angalamule phiri ili kuti, ‘Pita, kadziponye mʼnyanja,’ ndipo wosakayika mu mtima mwake koma kukhulupirira kuti chimene akunena chidzachitika, chidzachitikadi kwa iyeyo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndithu ndinena ndi inu, kuti, Munthu ali yense akanena ndi phiri ili, Tanyamulidwa, nuponyedwe m'nyanja; wosakayika mumtima mwace, koma adzakhulupirira kuti cimene acinena cicitidwa, adzakhala naco.