Mark 11:25 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndipo pamene mukuti mupemphere, muziyamba mwakhululukira mnzanu ngati muli naye nkanthu. Mukatero, Atate anunso amene ali Kumwamba adzakukhululukirani machimo anu.” [
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo pamene muimirira ndi kupemphera, khululukirani, ngati munthu wakulakwirani kanthu; kuti Atate wanunso ali Kumwamba akhululukire inu zolakwa zanu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pamene muyimirira kupemphera, ngati muli ndi chifukwa ndi wina, mukhululukireni, kuti Atate anu akumwamba akukhululukireni machimo anu.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo pamene muimirira ndi kupemphera, kholulukirani, ngati munthu wakulakwirani kanthu; kuti Atate wanunso ali Kumwamba akhulolukire inu zolakwa zanu.