Mark 11:27 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Yesu adafikanso ku Yerusalemu. Tsono pamene Iye ankangodziyendera m'Nyumba ya Mulungu, akulu a ansembe ndi aphunzitsi a Malamulo pamodzi ndi akulu a Ayuda adadzamufunsa kuti,
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo iwo anadzanso ku Yerusalemu; ndipo m'mene Iye anali kuyenda m'Kachisi, anafika kwa Iye ansembe aakulu, ndi alembi ndi akulu;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iwo anafikanso ku Yerusalemu, ndipo pamene Yesu amayenda mʼmabwalo a Nyumba ya Mulungu, akulu a ansembe, aphunzitsi amalamulo ndi akuluakulu anabwera kwa Iye.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo iwo anadzanso ku Yerusalemu; ndipo m'mene Iye anali kuyenda m'Kacisi, anafika kwa Iye ansembe akuru, ndi alembi ndi akuru;