Mark 12:1 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Yesu adayamba kulankhula nawo m'mafanizo. Adati, “Munthu wina adaabzala mipesa m'munda mwake, namanga mpanda kuzinga mundawo. Adakumba nkhuti yoponderamo mphesa, namanga nsanja yolondera mundawo. Pambuyo pake munda uja adaubwereka alimi, iye nkunyamuka ulendo wa ku dziko lina.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Iye anayamba kulankhula nao m'mafanizo. Munthu analima munda wamphesa, nauzunguniza ndi linga, nakumba moponderamo mphesa, namanga nsanja, naukongoletsa kwa olima munda, namuka kwina.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kenaka Iye anayamba kuyankhula nawo mʼmafanizo: “Munthu wina analima munda wamphesa. Anamanga mpanda mozungulira, nakumba dzenje lofinyiramo mphesa ndipo anamanga nsanja. Anawubwereketsa munda wamphesawo kwa alimi ena napita ku dziko lina.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Iye anayamba kulankhula nao m'mafanizo. Munthu analima munda wamphesa, nauzunguniza ndi linga, nakumba moponderamo mphesa, namanga nsanja, naukongoletsa kwa olima munda, namuka kwina.