Mark 12:10 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nanga monga simudaŵerenge Malembo aja akuti, “ ‘Mwala umene amisiri omanga nyumba adaaukana, womwewo wasanduka mwala wapangondya, wofunika koposa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Kodi simunawerenga ngakhale lembo ili, Mwala umene anaukana omanga nyumba, womwewu unayesedwa mutu wa pangodya:
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kodi simunawerenge lemba lakuti: “ ‘Mwala umene amisiri omanga nyumba anawukana wakhala mwala wa pa ngodya.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Kodi simunawerenga ngakhale lembo ili; Mwala umene anaukana omanga nyumba, Womwewu unayesedwa mutu wa pangondya: