Mark 12:14 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Atafika, adati, “Aphunzitsi, tikudziŵa kuti Inu mumanena zoona, ndipo simuwopa munthu aliyense. Simuyang'anira kuti uyu ndani, koma mumaphunzitsa malamulo a Mulungu moona. Nanga tsono, kodi Malamulo a Mulungu amalola kuti tizikhoma msonkho kwa Mfumu ya ku Roma, kapena ai?
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo pamene anafika, ananena naye, Mphunzitsi, tidziwa kuti muli woona, ndipo simusamala munthu; pakuti simuyang'ana nkhope ya anthu, koma muphunzitsa njira ya Mulungu moona: Nkuloleka kodi kupereka msonkho kwa Kaisara, kapena iai?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iwo anabwera kwa Iye nati, “Aphunzitsi, ife tikudziwa kuti Inu ndi munthu amene mumanena zoona. Inu simutengeka ndi anthu, chifukwa simusamala kuti ndi ndani; koma mumaphunzitsa njira ya Mulungu molingana ndi choonadi. Kodi ndi koyenera kupereka msonkho kwa Kaisara kapena ayi?
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika