Mark 12:15 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kodi tizikhomadi kapena tisamakhoma?” Koma Yesu podziŵa maganizo ao onyenga, adati, “Bwanji kodi mukundiyesa dala? Tandipatsirani ndalama, ntaiwona.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Kodi tipereke kapena tisapereke? Koma Iye anadziwa chinyengo chao, nati kwa iwo, Mundiyeseranji? Nditengereni rupiya latheka, kuti ndilione. Ndipo analitenga.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kodi ife tipereke msonkho kapena ayi?” Koma Yesu anadziwa chinyengo chawo. Iye anafunsa kuti, “Bwanji mukufuna kundipeza chifukwa? Bweretsani ndalama kuti ndiyione.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Kodi tipereke kapena tisapereke? Koma Iye anadziwa cinyengo cao, nati kwa iwo, Mundiyeseranji? Nditengereni rupiya latheka, kuti ndilione. Ndipo analitenga.