Mark 12:2 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nyengo yothyola zipatso itafika, munthu uja adatuma wantchito wake kwa alimi aja, kuti alimiwo akampatsireko zipatso za m'munda muja.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo m'nyengo yake anatuma kapolo kwa olimawo, kuti alandireko kwa olimawo zipatso za m'munda wamphesa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pa nthawi yokolola anatumiza wantchito kwa alimiwo kuti akatenge kuchokera kwa iwo zina mwa zipatso za munda wamphesa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo m'nyengo yace anatuma kapolo kwa olimawo, kuti alandireko kwa olimawo zipatso za m'munda wamphesa.