Mark 12:26 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono zakuti anthu adzauka kwa akufa, kodi simudaŵerenge m'buku la Mose, paja akunena za chitsamba choyakapa? Suja akuti Mulungu adamuuza Mose kuti, ‘Ine ndine Mulungu wa Abrahamu, ndine Mulungu wa Isaki, ndine Mulungu wa Yakobe?’
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
simunawerenga m'buku la Mose kodi, za chitsambacho, kuti Mulungu anati kwa iye, nanena, Ine Ndine Mulungu wa Abrahamu, ndi Mulungu wa Isaki, ndi Mulungu wa Yakobo?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsopano kunena zakuti akufa amauka, kodi simunawerenge mʼbuku la Mose, pa nkhani yachitsamba choyaka moto, mmene Mulungu anati kwa iye, ‘Ine ndine Mulungu wa Abrahamu, Mulungu wa Isake, ndi Mulungu wa Yakobo?’
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
simunawerenga m'kalata wa Mose kodi, za Citsambaco, kuti Mulungu anati kwa iye, nanena, Ine Ndine Mulungu wa Abrahamu, ndi Mulungu wa Isake, ndi Mulungu wa Yakobo?