Mark 12:28 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mphunzitsi wina wa Malamulo adaŵamva akutsutsana. Ataona kuti Yesu waŵayankha bwino Asaduki aja, adadza pafupi, namufunsa kuti, “Kodi mwa malamulo onse, lalikulu ndi liti?”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anadza mmodzi wa alembi, namva iwo alikufunsana pamodzi, ndipo pakudziwa kuti anawayankha bwino, anamfunsa Iye, Lamulo la m'tsogolo la onse ndi liti?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mmodzi wa aphunzitsi amalamulo anabwera namva iwo akukambirana motsutsana. Poona kuti Yesu anawapatsa yankho labwino, anamufunsa Iye kuti, “Mwa malamulo onse, kodi lopambana koposa ndi liti?”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anadza mmodzi wa alembi, namva iwo alikufunsana pamodzi, ndipo pakudziwa kuti anawayankha bwino, anamfunsa Iye, Lamulo la m'tsogolo la onse ndi liti?