Mark 12:33 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mwalondolanso ponena kuti chinthu chopambana ndicho kumkonda Mulungu ndi mtima wonse, ndi nzeru zonse, ndi mphamvu zonse, ndiponso kukonda mnzako monga umadzikondera iwe wemwe. Kuteroko nkoposa kupereka nsembe zopsereza ndiponso nsembe zina zonse.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ndipo, kumkonda Iye ndi mtima wonse, ndi nzeru yonse, ndi mphamvu yonse, ndi kukonda mnzake monga adzikonda mwini, ndiko kuposa nsembe zopsereza zamphumphu zonse, ndi nsembe zophedwa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kumukonda Iye; ndi mtima wako wonse, ndi nzeru zako zonse, ndi mphamvu zako zonse, ndi kukonda mnansi wako monga iwe mwini, ndi zopambana kuposa zopereka ndi nsembe zopsereza.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ndipo, kumkonda Iye ndi mtima wonse, ndi nzeru yonse, ndi mphamvu yonse, ndi kukonda mnzace monga adzikonda mwini, ndiko kuposa nsembe zopsereza zamphumphu zonse, ndi nsembe zophedwa.