Mark 12:34 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Yesu adaona kuti munthuyo wayankha mwanzeru. Tsono adamuuza kuti, “Iwe suli kutali ndi Ufumu wa Mulungu.” Ndipo kuyambira apo panalibenso wina woti ayesere kumfunsa kanthu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo pakuona kuti anayankha ndi nzeru, Yesu anati kwa iye, Suli kutali ndi Ufumu wa Mulungu. Ndipo palibe munthu analimbanso mtima kumfunsa Iye kanthu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yesu ataona kuti wayankha mwanzeru, anati kwa iye, “Iwe suli kutali ndi ufumu wa Mulungu.” Ndipo kuyambira pamenepo panalibe ndi mmodzi yemwe anayesa kumufunsanso.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo palmona kuti anayankha ndi nzeru, Yesu anati kwa iye, Suli kutali ndi Ufumu wa Mulungu. Ndipo palibe munthu analimbanso mtima kwnfunsa Iye kanthu.