Mark 12:37 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Davide weniweniyo akutchula Mpulumutsi wolonjezedwa uja kuti Mbuye wake. Tsono angakhale mwana wakenso bwanji?” Anthu ambirimbiri aja ankakondwa kwambiri pomva mau ake.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Davide mwini yekha amtchula Iye Ambuye; ndipo ali mwana wake bwanji? Ndipo anthu a makamuwo anakondwa kumva Iye.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Davide mwini wake amutchula Iye, ‘Ambuye.’ Nanga angakhale bwanji mwana wake?” Gulu lalikulu la anthu linamvetsera ndi chisangalalo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Davide mwini yekha amchula Iye Ambuye; ndipo ali mwana wace bwanji? Ndipo anthu a makamuwo anakondwa kumva Iye.