Mark 12:38 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pamene Yesu ankaŵaphunzitsa, adati, “Chenjera nawoni aphunzitsi a Malamulo. Amakonda kuyenda atavala mikanjo yaitali, ndi kuti anthu aziŵalonjera mwaulemu pa misika.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo m'chiphunzitso chake ananena, Yang'anirani mupewe alembi, akufuna kuyendayenda ovala miinjiro, ndi kulonjeredwa pamisika,
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pamene ankaphunzitsa, Yesu anati, “Samalani ndi aphunzitsi a malamulo. Amakonda kuyendayenda atavala mikanjo ikuluikulu ndi kumalonjeredwa mʼmisika.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo m'ciphunzitso cace ananena, Yang'anirani mupewe alembi, akufuna kuyendayenda obvala miinjiro, ndi kulankhulidwa pamisika,