Mark 12:41 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsiku lina Yesu adaakhala pansi kuyang'anana ndi bokosi loponyamo ndalama zopereka ku Nyumba ya Mulungu. Ankayang'anitsitsa m'mene anthu ankaponyera ndalama zao. Anthu ambiri achuma ankaponyamo ndalama zambiri.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Iye anakhala pansi pandunji pa mosungiramo ndalama, napenya kuti khamu la anthu alikuponya ndalama mosungiramo; ndipo eni chuma ambiri anaponyamo zambiri.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yesu anakhala pansi moyangʼanana ndi pamene amaperekera zopereka ndipo amaona anthu akupereka ndalama zawo mʼthumba la Nyumba ya Mulungu. Anthu ambiri olemera anaponya ndalama zambiri.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Iye anakhala pansi pandunji pa mosungiramo zopereka, napenya kuti khamu la anthu alikuponya ndalama mosungiramo; ndipo eni cuma ambiri anaponyamo zambiri.