Mark 12:44 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chifukwa ena onseŵa angoponyamo zimene atapa pa zochuluka zimene ali nazo. Koma maiyu, mwa umphaŵi wake, waponyamo zonse zimene anali nazo, ngakhale zimene akadagulira chakudya.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
pakuti anaponyamo onse mwa zochuluka zao; koma iye anaponya mwa kusowa kwake zonse anali nazo, inde moyo wake wonse.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iwo apereka molingana ndi chuma chawo; koma iye, mwaumphawi wake, wapereka zonse anali nazo ngakhale zoti akanagulira chakudya.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
pakuti anaponyamo onse mwa zocuruka zao; koma iye anaponya mwa kusowa kwace zonse anali nazo, inde moyo wace wonse.