Mark 13:11 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono akadzakugwirani ndi kukuperekani ku mlandu, musadzaderetu nkhaŵa nkumaganiza kuti, ‘Kodi tikanene chiyani?’ Ai, inu mukangonena zimene Mulungu akakuuzeni pa nthaŵi imeneyo. Pajatu odzalankhula sindinu ai, koma Mzimu Woyera.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo pamene adzapita nanu kumlandu, nadzakuperekani, musade nkhawa usanayambe mlandu ndi chimene mudzalankhula; koma chimene chidzapatsidwa kwa inu m'mphindi yomweyo, muchilankhule; pakuti olankhula si ndinu, koma Mzimu Woyera.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Nthawi iliyonse pamene mwamangidwa ndi kuyimbidwa mlandu, musadandaule za zimene mudzanena. Zimene mudzapatsidwe pa nthawiyo yankhulani; pakuti sindinu amene mudzayankhula, koma Mzimu Woyera.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo pamene adzapita nanu kumlandu, nadzakuperekani, musada nkhawa usanayambe mrandu ndi cimene mudzalankhula; koma ci mene cidzapatsidwa kwa inu m'mphindi yomweyo, mucilankhule; pakuti olankhula si ndinu, koma Mzimu Woyera.