Mark 13:19 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
chifukwa masautso amene adzaoneke masiku amenewo, sanaonekepo chilengedwere dziko lapansi mpaka pano, ndipo sadzaonekanso.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti masiku aja padzakhala chisautso, chonga sichinakhala chinzake kuyambira chiyambi cha chilengedwe chimene Mulungu anachilenga ndi kufikira tsopano, ndipo sichidzakhalanso, nthawi zonse.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
chifukwa masiku amenewo adzakhala owawitsa osafanana ndi ena kuyambira pachiyambi, pamene Mulungu analenga dziko, kufikira lero ndipo sadzafanananso ndi ena.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti masiku aja padzakhala cisautso, conga sicinakhala cinzace kuyambira ciyambi ca cilengedwe cimene Mulungu anacilenga ndi kufikira tsopano, ndipo sicidzakhalanso nthawi zonse.