Mark 13:20 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsonotu masiku amenewo, Ambuye akadapanda kuŵachepetsa, sakadapulumukapo munthu ndi mmodzi yemwe. Koma masikuwo Mulungu adaŵachepetsa chifukwa cha anthu omwe Iye adaŵasankha.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Ambuye akadapanda kufupikitsa masikuwo, sakadapulumuka munthu mmodzi yense; koma chifukwa cha osankhidwa amene anawasankha, anafupikitsa masikuwo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ambuye akanapanda kufupikitsa masikuwo, palibe amene akanapulumuka. Koma chifukwa cha osankhidwiratu, amene anawasankha, Iye anawafupikitsa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Ambuye akadapanda kufupikitsa masikuwo, sakadapulumuka munthu mmodzi yense; koma cifukwa ca osankhidwa amene anawasankha, anafupikitsa masikuwo.