Mark 13:27 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono Iye adzatuma angelo ake kuti akasonkhanitse osankhidwa ake kuchokera ku mbali zonse, kuyambira ku malekezero ena a dziko lapansi mpaka ku malekezero ake enanso.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo pamenepo adzatuma angelo, nadzasonkhanitsa osankhidwa ake ochokera kumphepo zinai, kuyambira ku malekezero ake a dziko lapansi, ndi kufikira ku malekezero a thambo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo adzatuma angelo ake kukasonkhanitsa osankhidwiratu ake ku mphepo zinayi, kuyambira kumalekezero a dziko lapansi mpaka ku malekezero ake enanso.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo pamenepo adzatuma angelo, nadzasonkhanitsa osankhidwa ace ocokera ku mphepo zinai, kuyambira ku malekezero ace a dziko lapansi, ndi kufikira ku malekezero a thambo.