Mark 13:34 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndi monga ngati bwana amene akunyamuka ulendo kuchoka kunyumba kwake. Amasiya zinthu m'manja mwa antchito ake, aliyense ntchito yake, ndipo amauza wapakhomo kuti azikhala maso.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Monga ngati munthu wa paulendo, adachoka kunyumba kwake, nawapatsa akapolo ake ulamuliro, kwa munthu aliyense ntchito yake, nalamula wapakhomo adikire.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Zili ngati munthu amene akuchokapo. Amasiyira nyumba yake antchito ake, aliyense ndi ntchito yake; ndi kumuwuza wa pa khomo kuti azikhala maso.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Monga ngati munthu wa paulendo, adacoka kunyumba kwace, nawapatsa akapolo ace ulamuliro, kwa munthu ali yense nchito yace, nalamulira wapakhomo adikire.