Mark 13:7 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma inu mukadzamva phokoso la nkhondo za kufupi kuno, kapena mphekesera za nkhondo zakutali, musadzade nkhaŵa ai. Zimenezi zidzayenera kuchitika, koma sindiye kuti chimalizo chija chafika kale ai.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo m'mene mudzamva za nkhondo ndi mbiri zake za nkhondo, musamadera nkhawa: ziyenera kuchitika izi; koma sichinafike chimaliziro.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pamene mudzamva zankhondo ndi mbiri zankhondo, musadzadzidzimuke. Zinthu zotere ziyenera kuchitika, koma sikuti chimaliziro chafika kale ayi.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo m'mene mudzamva za nkhondo ndi mbiri zace za nkhondo, musamadera nkhawa: ziyenerakucitika izi; koma sicinafike cimariziro.