Mark 13:9 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Koma inu muchenjere. Anthu adzakuperekani ku mabwalo amilandu a Ayuda, ndipo adzakukwapulani m'nyumba zao zamapemphero. Mudzaonekera kwa akulu a Boma ndi kwa mafumu chifukwa cha Ine, kuti mukandichitire umboni pamaso pao.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma inu mudziyang'anire inu nokha; pakuti adzakuperekani inu kwa akulu a milandu; ndipo adzakukwapulani m'masunagoge; ndipo pamaso pa akazembe ndi mafumu mudzaimirira chifukwa cha Ine, kukhale umboni kwa iwo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Muyenera kukhala tcheru. Mudzaperekedwa ku mabwalo oweruza ndi kukwapulidwa mwankhanza mʼmasunagoge. Mudzayima pamaso pa abwanamkubwa ndi mafumu monga mboni kwa iwo chifukwa cha Ine.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma inu mudziyang'anire inu nokha; pakuti adzakuperekani inu kwa akuru a mirandu; ndipo adzakukwapulani m'masunagoge; ndipo pamaso pa akazembe ndi mafwnu mudzaimirira cifukwa ca Ine, kukhale umboni kwa iwo.