Mark 14:1 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kudangotsala masiku aŵiri kuti chifike chikondwerero cha Paska ndi chikondwerero cha masiku odya buledi wosafufumitsa. Akulu a ansembe ndi aphunzitsi a Malamulo ankafunafuna njira yoti amgwirire Yesu mochenjera, nkumupha.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo popita masiku awiri kuli phwando la Paska ndi mikate yopanda chotupitsa; ndipo ansembe aakulu ndi alembi anafunafuna momchitira chiwembu, ndi kumupha:
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsopano panali patatsala masiku awiri okha kuti tsiku la Paska ndi Phwando la Buledi wopanda yisiti lifike, ndipo akulu a ansembe ndi aphunzitsi amalamulo ankafunafuna mpata woti amugwire Yesu ndi kumupha.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo popita masiku awiri kuli phwando la Paskha ndi mikate yopanda cotupitsa; ndipo ansembe akuru ndi alembi anafunafuna momcitira ciwembu, ndi kumupha: