Mark 14:12 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pa tsiku loyamba la masiku a buledi wosafufumitsa, tsiku lomwe anthu ankapha mwanawankhosa wochitira phwando la Paska, ophunzira a Yesu adamufunsa kuti, “Kodi tikakukonzereni kuti malo okadyerako phwando la Paska?”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo tsiku loyamba la mikate yopanda chotupitsa, pamene amapha Paska, ophunzira ananena naye, Mufuna tinke kuti, tikakonze mkadyereko Paska?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pa tsiku loyamba la Phwando la Buledi wopanda yisiti, nthawi imene mwa mwambo inali ya kupha mwana wankhosa wa Paska, ophunzira a Yesu anafunsa Iye kuti, “Mufuna tipite kuti kumene tikakonzekere kuti mukadyere Paska?”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo tsiku loyamba la mikate yopanda cotupitsa, pamene amapha Paskha, ophunzira ace ananena naye, Mufuna tinke kuti, tikakonze mkadyereko Paskha?