Mark 14:25 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kunena zoona, sindidzamwanso chakumwa cha mtengo wamphesachi, mpaka tsiku limene ndidzamwe chatsopano mu Ufumu wa Mulungu.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo ndinena nanu, Sindidzamwanso chipatso cha mpesa, kufikira tsiku lijalo, limene ndidzamwa icho chatsopano mu Ufumu wa Mulungu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Zoonadi, ndikuwuzani kuti sindidzamwanso kuchokera ku chipatso cha mphesa mpaka tsikulo pamene ndidzamwa chatsopano mu ufumu wa Mulungu.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndithu ndinena nanu, Sindidzamwanso cipatso ca mpesa, kufikira tsiku lijalo, limene ndidzamwa ico catsopano mu Ufumu wa Mulungu.