Mark 14:3 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsiku lina Yesu anali ku Betaniya, m'nyumba ya Simoni wotchedwa Wakhate. Pamene ankadya, kudafika mai wina atatenga nsupa yagalasi ya mafuta enieni onunkhira, amtengowapatali, a mtundu wa narido. Maiyo adaphwanya nsupa ija, nayamba kuthira mafutawo pamutu pa Yesu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo pakukhala Iye ku Betaniya m'nyumba ya Simoni wakhate, m'mene anaseama kudya, anadzapo mkazi ali nayo nsupa ya alabastero ya mafuta onunkhira bwino a narido weniweni a mtengo wapatali; naswa nsupayo, nawatsanulira pamutu pake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pamene Iye anali mʼBetaniya, atakhala pa tebulo akudya mʼnyumba ya munthu wodziwika kuti Simoni wakhate, anabwera mayi ndi botolo la mafuta onunkhira amtengo wapamwamba opangidwa ndi nadi. Anaphwanya botololo nakhuthula mafutawo pa mutu wa Yesu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo pakukhala iye ku Betaniya m'nyumba ya Simoni wakhate, m'mene anaseama kudya, anadzapo mkazi ali nayo nsupa yaalabastero ya mafuta onunkhira bwino a nardo weni weni a mtengowapatali; naswa nsupayo, nawatsanulira pamutu pace.