Mark 14:40 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pamene adabwerakonso, adaŵapeza ali m'tulo, chifukwa zikope zao zinkalemera ndi tulo. Choncho iwowo adasoŵa choyankha.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anadzanso nawapeza ali m'tulo, pakuti maso ao analemeradi; ndipo sanadziwe chomyankha Iye.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iye atabwerera, anawapezanso akugona, chifukwa mʼmaso mwawo munadzaza tulo. Iwo sanadziwe choti anene kwa Iye.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anadzanso nawapeza ali m'tulo, pakuti maso ao analemeradi; ndipo sanadziwa comyankha Iye.